Misonzi yachimwemwe idatsikira mmasaya mwa Sitelia kuchoka mmaso mwake. Sadathe kukhulupirira kuti loto lake lakwaniritsidwa. Zinali ngati kuti ali mtulo ndipo ali kulota. Chapatali potero Waisoni adakhala chete mkumaonerera mwambo wonse wa ukwati wa mkazi wake wa kale. Adakumbukira mmene amkamutukwanira komanso kumunyoza mkazi yo pa nthawi imene adali limodzi, mtima wake udagunda koposa ndipo anamva kuwawidwa. Kwa iye mkazi anali kalopo koposa ndipo amkakhulupirira kuti kumtchenetsa mkazi Kapena kumuyambitsa bizinesi kunali kutaya nthawi komanso kuononga ndalama chabe. Tsiku liri lonse Sitelia adali akukhala odandaula ndinso kugona ndi njala limodzi ndi ana ake awiri pamene Waisoni adali kupita kuzisangalalo kumene amakadyako mang'ina, zibwente, tchipisi ndi fuloze. Amkapita kunyumba atakhuta ndipo amkangofikira phiii kugona. Khalidwe li mkazi atafika potopa nalo anayamba kuyenda yenda mnamakasaka chakudya cha iye ndi ana ake ndipo waisoni analibe nazo ntchito. Pamene mkazi yu ada...
Short Stories, Articles, Book Series, Poems, Proses, Affirmations

Comments
Post a Comment