Misonzi yachimwemwe idatsikira mmasaya mwa Sitelia kuchoka mmaso mwake. Sadathe kukhulupirira kuti loto lake lakwaniritsidwa. Zinali ngati kuti ali mtulo ndipo ali kulota. Chapatali potero Waisoni adakhala chete mkumaonerera mwambo wonse wa ukwati wa mkazi wake wa kale. Adakumbukira mmene amkamutukwanira komanso kumunyoza mkazi yo pa nthawi imene adali limodzi, mtima wake udagunda koposa ndipo anamva kuwawidwa. Kwa iye mkazi anali kalopo koposa ndipo amkakhulupirira kuti kumtchenetsa mkazi Kapena kumuyambitsa bizinesi kunali kutaya nthawi komanso kuononga ndalama chabe. Tsiku liri lonse Sitelia adali akukhala odandaula ndinso kugona ndi njala limodzi ndi ana ake awiri pamene Waisoni adali kupita kuzisangalalo kumene amakadyako mang'ina, zibwente, tchipisi ndi fuloze. Amkapita kunyumba atakhuta ndipo amkangofikira phiii kugona. Khalidwe li mkazi atafika potopa nalo anayamba kuyenda yenda mnamakasaka chakudya cha iye ndi ana ake ndipo waisoni analibe nazo ntchito. Pamene mkazi yu adakali pakati posaka chakudya adakumana ndi chikhwaya chogwira ntchito mu banki, adakondana ndipo ubwenzi udayamba. Kwa miyezi ingapo ubwenzi wawo udakulira ndinso kutentherera koma zonsezi Waisoni sadali kuziwa pakuti samkakhala pakhomo tsiku lonse. Usiku wina mwachidzolowedzi adangodabwa kufika pakhomo mkupedza kuti mkazi wake komanso ana palibe. Adayang'ana muzipinda zonse za mnyumba mo ndipo sadawapedze, adakhala pabalaza mnawadikirira koma mawola awiri adadutsa ndipo iwo sadatulukire, adaganiza zopita kuchipinda kumene iye ndi mkazi wake Sitelia amkagona ndipo adali ozizidwa nkhongono kupedza chibaluwa chomwe mkazi yo adalemba kumusanzika kuti wapita kukaona patsidya la nyanja pamodzi ndi khadi lomuitana ku ukwati omwe mkazi wakeyo adali kuchita lachiweru lomwe lidali kudza. Izi zinamuvuta Waisoni kukhulupirira ndipo lisipa ndi mutu wa ching'alang'ala zidamupedza. Adakanika kumvetsa kuti mkazi wakeyo wapitadi ndipo adawona kuchedwa kuti lachiweru lifike akazionere yekha ngati zinalidi zoona. Tulo tidamusowa. Adakhala akulingalira komanso Kulira kuti zibwana zake zamuthawitsira mkazi ndi ana omwe. Tsiku lo litafika Wasioni adakonzeka molawira koposa ngati mwina ukwati wo udali wake ndipo adalunjika Ku kachisi imene ukwati wo umkadalitsidwira. Mmimba mudaotcha ndipo adaona ngati chifunga komanso anamva kutentha mthupi mwake monse pamene adawona mkazi wake Sitelia ali mu Velo loyera bwino ngati ngelo, maphodedwe amene adali pa thupi la mkazi yu adamupangitsa Waisoni kubwera mkhwidzi yomwe adakanika kuitula pakuti kupusa kwake mkomwe kudapangitsa kuti ena amulande mkazi. Adalaka laka atatsatira mkazi wake yo kutsogolo pamene m'busa adafunsa ngati analipo wina oletsa kuti awiri wo asakhale limodzi ngati banja. Koma kunali komuvuta zedi Waisoni kutero pakuti miyendo yake komanso minyewa yonse idali itafooka koposa ndipo mphamvu zoimirira adalibe pakuti adali kuopa kuti atha kuchitira chimbuzi mukachisi mo kaamba ka mantha komanso mkwiyo ndi manyazi omwe adali nawo. Apa mpamene Waisoni adadzindikira kuti munthu di akapusa amadyeredwa ndithu ingakhale mkazi amene.. CHENJERA!!!!
THE END!
Wow!!! You have put a lot of work into this piece and phunziro lalikulu heavy. Keep up the good work 💪💪💪
ReplyDeleteThanks so much!
DeleteWill surely hang on!!